Masamu kuchionetsero
Lulu ali kuchionetsero ndi kalasi lake la ophunzira 36. Koma aphunzitsi ayenera kuwawerengera kuti aone matikiti amene afunikira kugula ndipo kuchita chotheka kuti ngakhale mwana mmodzi asasowe. Kodi kuli njira yapafupi imene anthe kugwiritsa nchito pa kuwerengera 36 kupambana 1,2,3...? Ganiziro la matebulo libweretsedwa kupitira munkhani ya kuwerengera m'magulu.