Tanje Wamkulu
Musuku anakolola zambiri kucoka m’munda ndipo anaika zokolola zake munkokwe. Anaika tanje wamkulu pamwamba kuti abise zonse zomwe zinali mnkokwe ndi kulemba cona nchito yokhala malonda. Tanje uyu anali wamkulu womwe sauonepo m’mudzi wa Musuku. Ambiri anakhala ndi cidwi ndi tanje uyu maka-maka nyani omwe anali mbala. Kodi muganiza kuti cona azateteza tanje ndi zokolola zina zonse?